komatu sindidzachotsa ufumu wonsewo; fuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi chifukwa cha Yerusalemu amene ndinamsankha.
Nehemiya 11:18 - Buku Lopatulika Alevi onse m'mzinda wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Alevi onse m'mudzi wopatulikawo ndiwo mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu kudza anai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Alevi onse amene ankakhala mu mzinda wopatulika analipo 284 pamodzi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Alevi onse amene anali mu mzinda woyera analipo 284. |
komatu sindidzachotsa ufumu wonsewo; fuko limodzi ndidzapatsa mwana wako, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndi chifukwa cha Yerusalemu amene ndinamsankha.
Ndipo akulu a anthu anakhala mu Yerusalemu; anthu otsala omwe anachita maere, kuti libwere limodzi la magawo khumi likhale mu Yerusalemu, mzinda wopatulika, ndi asanu ndi anai akhumi m'mizinda ina.
ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.
Ndi odikira: Akubu, Talimoni, ndi abale ao akulindira pazipata, ndiwo zana limodzi mphambu makumi asanu ndi awiri kudza awiri.
Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.
Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)
ndipo anatuluka m'manda mwao pambuyo pa kuuka kwake, nalowa m'mzinda woyera, naonekera kwa anthu ambiri.
Pamenepo mdierekezi anamuka naye kumzinda woyera; namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisi,
Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.
Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika Kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake.