Ndipo wa Alevi, Ahiya anayang'anira chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi chuma cha zopatulika.
Nehemiya 11:16 - Buku Lopatulika ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akulu a Alevi, anayang'anira ntchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi Sabetai, ndi Yozabadi, mwa akulu a Alevi, anayang'anira ntchito za pabwalo za nyumba ya Mulungu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sabetai ndiponso Yozabadi anali atsogoleri a Alevi amene ankayang'anira ntchito ya kunja kwa Nyumba ya Mulungu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sabetayi ndi Yozabadi anali atsogoleri amene ankayangʼanira ntchito ya kunja kwa Nyumba ya Mulungu. |
Ndipo wa Alevi, Ahiya anayang'anira chuma cha nyumba ya Mulungu, ndi chuma cha zopatulika.
A Aizihara: Kenaniya ndi ana ake anachita ntchito ya pabwalo ya Israele, akapitao ndi oweruza milandu.
Yonatani mwana wa Asahele ndi Yazeya mwana wa Tikiva okha anatsutsana nacho, ndi Mesulamu ndi Sabetai Mlevi anawathandiza.
Ndipo pa tsiku lachinai siliva ndi golide ndi zipangizo zinayesedwa m'nyumba ya Mulungu wathu, m'dzanja la Meremoti mwana wa Uriya wansembe, ndi pamodzi naye Eleazara mwana wa Finehasi, ndi pamodzi nao Yozabadi mwana wa Yesuwa, ndi Nowadiya mwana wa Binuyi, Alevi;
Ndi mwa Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni;
ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, ndiye mkulu wakuyamba mayamiko, popemphera; ndi Bakibukiya wotsatana naye mwa abale ake, ndi Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.
Ndi Yesuwa, ndi Bani, ndi Serebiya, Yamini, Akubu, Sabetai, Hodiya, Maaseiya, Kelita, Azariya, Yozabadi, Hanani, Pelaya, ndi Alevi, anadziwitsa anthu chilamulocho; ndi anthu anali chilili pamalo pao.