Nehemiya 11:13 - Buku Lopatulika ndi abale ake akulu a nyumba za makolo awiri mphambu makumi anai kudza awiri, ndi Amasisai mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndi abale ake akulu a nyumba za makolo awiri mphambu makumi anai kudza awiri, ndi Amasisai mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndiponso achibale ao amene anali akuluakulu a banja lao. Onse pamodzi analipo 242. Amasisai, mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndi abale ake, amene anali atsogoleri a mabanja. Onse pamodzi anali 242. Kuphatikiza apo panalinso Amasisai mwana wa Azaireli, mwana wa Ahazayi, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri |
ndi abale ao ochita ntchito ya m'nyumbayi ndiwo mazana asanu ndi atatu mphambu makumi awiri kudza awiri; ndi Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya;
ndi abale ao, ngwazi zamphamvu, zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi atatu; ndi woyang'anira wao ndiye Zabidiele mwana wa Hagedolimu.