ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.
Nehemiya 10:32 - Buku Lopatulika Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tinadziikiranso malamulo, kuti tizipereka chaka ndi chaka limodzi la magawo atatu a sekeli kuntchito ya nyumba ya Mulungu wathu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tikulumbiranso kuti chaka ndi chaka tizipereka magaramu anai a siliva, kuti tithandize pa ntchito za ku Nyumba ya Mulungu wathu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tikulonjezanso molumbira kuti chaka ndi chaka tizipereka magalamu anayi a siliva kuti zithandize ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu wathu. |
ndi mwala umenewu ndinauimiritsa, udzakhala nyumba ya Mulungu; ndipo la zonse mudzandipatsa ine, ndidzakupatsani Inu limodzi la magawo khumi.
Masiku awa ndinaona ku Yuda ena akuponda mphesa m'choponderamo tsiku la Sabata, ndi akubwera nayo mitolo ya tirigu, ndi kuisenzetsa pa abulu; momwemonso vinyo, mphesa, ndi nkhuyu, ndi zosenza zilizonse, zimene analowa nazo mu Yerusalemu tsiku la Sabata, ndipo ndinawachitira umboni wakuwatsutsa tsikuli anagulitsa zakudya.
Sanatero kodi makolo anu, ndipo Mulungu wathu anatifikitsira ife ndi mzinda uno choipa ichi chonse? Koma inu muonjezera Israele mkwiyo pakuipsa Sabata.
Koma ndinawachitira umboni wakuwatsutsa, ndinanena nao, Mugoneranji pafupi pa linga? Mukateronso ndikuthirani manja. Kuyambira pomwepo sanafikenso pa Sabata.
Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndalama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili.
ndi Sabata lanu lopatulika munawadziwitsa, nimunawalamulira malamulo, ndi malemba, ndi chilamulo, mwa dzanja la Mose mtumiki wanu;
koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona.
Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.