Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu, pomchotsera moyo wake?
Mlaliki 9:4 - Buku Lopatulika Pakuti woyang'ana ndi amoyo onse ali nacho chiyembekezo; pakuti galu wamoyo aposa mkango wakufa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti woyang'ana ndi amoyo onse ali nacho chiyembekezo; pakuti galu wamoyo aposa mkango wakufa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe amene ali ndi moyo ali nacho chikhulupiriro. Paja akuti ndiponi galu wamoyo kuposa mkango wakufa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aliyense amene ali ndi moyo amakhala ndi chiyembekezo, pajatu galu wamoyo aposa mkango wakufa! |
Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu, pomchotsera moyo wake?
Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.
Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.
Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni; Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.