Mlaliki 8:6 - Buku Lopatulika pakuti kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chiweruzo chake; popeza zoipa za munthu zimchulukira; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chiweruzo chake; popeza zoipa za munthu zimchulukira; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi kachitidwe kake, ngakhale kuti mavuto ake a munthu amamupsinja kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti pali nthawi yoyenera ndiponso machitidwe a chinthu chilichonse, ngakhale kuti mavuto ake a munthu amupsinja kwambiri. |
Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m'njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziwitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi.
Kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake;
Chinthu chilichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m'mitima yao ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.
Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse.
Pamene atauka mwini nyumba natseka pakhomo, ndipo inu mudzayamba kuima pabwalo, ndi kugogoda pachitseko, ndi kunena, Ambuye titsegulireni ife; ndipo Iye adzayankha nadzati ndi inu, Sindidziwa inu kumene muchokerako;