Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
Mlaliki 8:2 - Buku Lopatulika Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m'kulumbira Mulungu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nditi, Sunga mau a mfumu, makamaka m'kulumbira Mulungu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Uzimvera lamulo la mfumu, ndipo chifukwa cha lumbiro lako kwa Mulungu usade nkhaŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ine ndikuti, mvera lamulo la mfumu, chifukwa unalumbira pamaso pa Mulungu. |
Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
Ndi akulu onse, ndi amuna amphamvu onse, ndi ana aamuna onse omwe a mfumu Davide, anagonjeratu kwa Solomoni mfumu.
lumbiro la Yehova likhale pakati pa iwo awiri, kuti sanatulutse dzanja lake pa chuma cha mnansi wake; ndipo mwiniyo azivomereza, ndipo asalipe.
Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa ntchito iliyonse yabwino;
Ndipo pakufika anthuwo m'nkhalangomo, onani, madzi a uchi anachuluka; koma panalibe munthu mmodzi anaika dzanja lake pakamwa, pakuti anthuwo anaopa tembererolo.