Mlaliki 7:8 - Buku Lopatulika Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake. Mtima wopirira ndi wopambana mtima wodzikuza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mathero ake a chinthu ndi abwino kupambana chiyambi chake, ndipo kufatsa nʼkwabwino kupambana kudzikuza. |
Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.
Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.
Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.
Mwa ichi, podzimanga m'chuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konsekonse chisomo chilikutengedwa kudza nacho kwa inu m'vumbulutso la Yesu Khristu;