Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
Mlaliki 7:6 - Buku Lopatulika Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mbiya. Zimenezinso nzachabechabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuseka kwa zitsiru kuli ngati kuthetheka kwa moto kunsi kwa mʼphika, izinso ndi zopandapake. |
Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula.
Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa, ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.
Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pamutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa.
Koma Abrahamu anati, Mwana, kumbukira kuti unalandira zokoma zako pakukhala m'moyo iwe, momwemonso Lazaro zoipa; ndipo tsopano iye asangalatsidwa pano, koma iwe uzunzidwadi.
Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.