Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
Mlaliki 7:5 - Buku Lopatulika Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuli bwino kuti munthu azimva kudzudzula kwa anthu anzeru, kupambana kumvera nyimbo zotamanda za zitsiru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuli bwino kumva kudzudzula kwa munthu wanzeru kusiyana ndi kumvera mayamiko a zitsiru. |
Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
Monga mphete yagolide ndi chipini chagolide woyengeka, momwemo wanzeru wodzudzula pa khutu lomvera.
Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika; ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.
Mau a anzeru akunga zisonga, omwe akundika mau amene mbusa mmodzi awapatsa mau ao akunga misomali yokhomedwa zolimba.
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.