Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mlaliki 7:4 - Buku Lopatulika

Mtima wa anzeru uli m'nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m'nyumba ya kuseka.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mtima wa anzeru uli m'nyumba ya maliro; koma mtima wa zitsiru uli m'nyumba ya kuseka.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mtima wa munthu wanzeru umalingalira kaŵirikaŵiri za imfa. Koma mtima wa munthu wopusa umalingalira za chimwemwe.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mtima wa munthu wanzeru nthawi zonse umalingalira za imfa, koma mitima ya zitsiru imalingalira za chisangalalo.

Onani mutuwo



Mlaliki 7:4
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu analamulira anyamata ake, nati, Inu mukhale maso, mtima wa Aminoni ukasekera ndi vinyo, ndipo ine ndikati kwa inu, Kanthani Aminoni; pamenepo mumuphe, musaope; sindine ndakulamulirani inu mulimbike, chitani chamuna.


Ndipo amenewo anatuluka usana. Koma Benihadadi analinkumwa naledzera m'misasamo, iye ndi mafumu aja makumi atatu mphambu awiri aja akumthandiza.


Ndinati mumtima mwanga, Tiyetu, ndikuyese ndi chimwemwe; tapenya tsono zabwino; ndipo taona, ichinso ndi chabe.


Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.


Kumva chidzudzulo cha anzeru kupambana kumva nyimbo ya zitsiru.


Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; chizirezire chimene ndinachikhumba chandisandukira kunthunthumira.


Pamene atentha, ndidzakonza madyerero ao, ndidzawaledzeretsa, kuti asangalale, agone chigonere, asanyamuke, ati Yehova.


Ndipo ndidzaledzeretsa akulu ake ndi anzeru ake, akazembe ake ndi ziwanga zake, ndi anthu ake olimba; ndipo adzagona chigonere, sadzanyamuka, ati Mfumu, dzina lake ndi Yehova wa makamu.


Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Ababiloni anaphedwa.


Tsiku la mfumu yathu akalonga adzidwalitsa ndi kutentha kwa vinyo; iye anatambasula dzanja lake pamodzi ndi oseka.


Pakuti chinkana akunga minga yoyangayanga, naledzera nacho choledzeretsa chao, adzathedwa konse ngati chiputu chouma.


Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha.


Ndipo pamene anatsika naye, onani, iwo anabalalika apo ponse, analinkudya, ndi kumwa, ndi kudyerera, chifukwa cha chofunkha zambiri anazitenga ku dziko la Afilisti, ndi ku dziko la Yuda.