Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.
Mlaliki 6:3 - Buku Lopatulika Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Munthu ngakhale abale ana zana limodzi, nkukhala ndi moyo zaka zambiri, ngakhale zaka zakezo zichuluke chotani, ngati sakondwerera zinthu zabwino za pa moyo wake, potsiriza osalandira maliro aulemu, ndithu ine ndikuti munthuyo ngakhale mtayo womwe umpambana kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngakhale munthu atabereka ana 100 ndi kukhala ndi moyo zaka zambiri; komatu ngakhale atakhala zaka zambiri chotani, ngati iye sangadyerere chuma chake ndi kuyikidwa mʼmanda mwaulemu, ine ndikuti mtayo umamuposa iyeyo. |
Ndipo anatukula maso ake nawaona akazi ndi ana; nati, Ndani awa ali ndi iwe? Ndipo iye anati, Ndiwo ana amene Mulungu anakomera mtima kumpatsa kapolo wanu.
Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.
Ndipo Ahabu anali nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri mu Samariya. Nalemba makalata Yehu, natumiza ku Samariya kwa akulu a Yezireele, ndiwo akuluakulu, ndi iwo adalera ana a Ahabu, ndi kuti,
Namuka iwo kuti amuike; koma sanapezeko kanthu kena koma bade, ndi mapazi, ndi zikhato za manja.
ndi mwa ana anga onse (pakuti Yehova wandipatsa ana aamuna ambiri), anasankha Solomoni mwana wanga akhale pa mpando wachifumu wa ufumu wa Yehova kuweruza Israele.
Ndipo Rehobowamu anakonda Maaka mwana wamkazi wa Abisalomu koposa akazi ake onse, ndi akazi ake aang'ono (pakuti adatenga akazi khumi mphambu asanu ndi atatu, ndi akazi aang'ono makumi asanu ndi limodzi, nabala ana aamuna makumi awiri mphambu asanu ndi atatu, ndi ana aakazi makumi asanu ndi limodzi).
Nawawerengera Hamani kulemera kwake kwakukulu, ndi ana ake ochuluka, ndi zonse mfumu idamkuza nazo, ndi umo adamkweza koposa akalonga ndi anyamata a mfumu.
inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone ntchito yoipa yochitidwa kunja kuno.
Chifukwa chake Yehova atero za Yehoyakimu mfumu ya Yuda: Adzasowa wokhala pa mpando wachifumu wa Davide; ndipo mtembo wake udzaponyedwa usana kunja kuli dzuwa, ndi usiku kuli chisanu.
ndipo udzawayanika padzuwa, ndi pamwezi, ndi pa khamu lonse la kuthambo, limene analikonda, ndi kulitumikira, ndi kulitsata, ndi kulifuna, ndi kuligwadira; sadzasonkhanidwa, sadzaikidwa; adzakhala ndowe panthaka.
Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.