Yakobo ndipo analumbira chilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m'njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zovalira za kuvala,
Mlaliki 5:4 - Buku Lopatulika Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ukalumbira chinthu kwa Mulungu, usachedwe kuchichita, chifukwa Mulungu sakondwera nazo zitsiru. Zimene wazilumbira, uzichitedi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako. |
Yakobo ndipo analumbira chilumbiro, nati, Mulungu akakhala ndi ine, akandisunga ine m'njira imene ndipitamo, akandipatsa ine mkate wa kudya, ndi zovalira za kuvala,
Ndipo Mulungu anati kwa Yakobo, Nyamuka nukwere kunka ku Betele nukhale kumeneko: numange kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anaonekera kwa iwe pamene unathawa ku nkhope ya Esau mbale wako.
tinyamuke, tikwere tinke ku Betele: ndipo tidzamanga kumeneko guwa la nsembe la Mulungu amene anandivomereza tsiku la mavuto anga, ndiponso anali ndi ine m'njira m'mene ndinapitamo.
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
Windani ndipo chitirani Yehova Mulungu wanu zowindazo; onse akumzinga abwere nacho chopereka cha kwa Iye amene ayenera kumuopa.
Kunena mwansontho, Ichi nchopatulika, kuli msampha kwa munthu, ndi kusinkhasinkha pambuyo pake atawinda.
Ndipo Yehova adzadziwika kwa Ejipito, ndipo Aejipito adzadziwa Yehova tsiku limenelo; inde iwo adzapembedzera ndi nsembe ndi zopereka, nadzawindira Yehova ndi kuchitadi.
Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika, ndidzakwaniritsa chowinda changa. Chipulumutso ncha Yehova.
Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe paguwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m'dzanja lanu.
Munthu akachitira Yehova chowinda, kapena akalumbira lumbiro ndi kumangira moyo wake chodziletsa, asaipse mau ake; azichita monga mwa zonse zotuluka m'kamwa mwake.
Ndiponso, munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usalumbire konama, koma udzapereka kwa Ambuye zolumbira zako:
Ndipo kunali, pakumuona anang'amba zovala zake, nati, Tsoka ine, mwana wanga, wandiweramitsa kwakukulu, ndiwe wa iwo akundisaukitsa ine; pakuti ndamtsegulira Yehova pakamwa panga ine, ndipo sinditha kubwerera.