Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mlaliki 4:9 - Buku Lopatulika

Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'ntchito zao.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Awiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m'ntchito zao.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kukhala aŵiri nkwabwino koposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu aŵiri ili ndi phindu lopambana.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha, chifukwa ntchito ya anthu awiri ili ndi phindu:

Onani mutuwo



Mlaliki 4:9
15 Mawu Ofanana  

Yehova Mulungu ndipo anati, Si kwabwino kuti munthu akhale yekha; ndidzampangira womthangatira iye.


Ndipo anati, Akandiposa mphamvu Aaramu, udzandilanditsa ndiwe; koma akakuposa mphamvu ana a Amoni, ndidzakulanditsa ndine.


Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.


Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake; koma tsoka wakugwa wopanda womnyamutsa.


Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.


Ndipo Yehova anautsa mzimu wa Zerubabele mwana wa Sealatiele, chiwanga cha Yuda, ndi mzimu wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi mzimu wa otsala onse a anthu, ndipo anadza nagwira ntchito m'nyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wao,


Sinditha kuwasenza anthu awa onse ndekha, pakuti andilemera ine.


Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;


Wakumweta alandira kulipira, nasonkhanitsira chobala kumoyo wosatha; kuti wofesayo akakondwere pamodzi ndi womwetayo.


Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.


Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.


Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.