Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena choipa chondigwera.
Mlaliki 3:8 - Buku Lopatulika mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana; mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mphindi yakukonda ndi mphindi yakudana; mphindi ya nkhondo ndi mphindi ya mtendere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pali nthaŵi yokondana ndi nthaŵi yodana, nthaŵi ya nkhondo ndi nthaŵi ya mtendere. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yokondana ndi nthawi yodana, nthawi ya nkhondo ndi nthawi ya mtendere. |
Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipumulitsa ku mbali zonse; palibe wotsutsana nane, kapena choipa chondigwera.
Ndipo kunali, pamene Yoramu anaona Yehu, anati, Mtendere kodi, Yehu? Nati iye, Ngwanji mtendere pokhala chachuluka chigololo ndi nyanga zake za mai wako Yezebele?
Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.
Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira.
Anasanduliza mitima yao, kuti adane nao anthu ake, kuti achite monyenga ndi atumiki ake.
Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu?
Ndipo popita Ine panali iwepo ndi kukupenya, taona nyengo yako ndiyo nyengo yakukondana; pamenepo ndinakufunda chofunda changa, ndi kuphimba umaliseche wako; inde ndinakulumbirira ndi kupangana nawe, ati Ambuye Yehova, ndipo unakhala wanga.
Munthu akadza kwa Ine, wosada atate wake ndi amake, ndi mkazi wake, ndi ana, ndi abale, ndi alongo ake, inde ndi moyo wake womwe wa iye mwini, sangathe kukhala wophunzira wanga.
ndi kuzama nchiyani; ndi kuzindikira chikondi cha Khristu, chakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira chidzalo chonse cha Mulungu.
Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Khristu anakonda Mpingo, nadzipereka yekha m'malo mwake;
Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israele, likhale cholowa chao, fuko lililonse gawo lake. Ndipo dziko linapumula nkhondo.
Ndidziwa ntchito zako, ndi chilemetso chako ndi chipiriro chako ndi kuti sungathe kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzitcha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;