Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.
Mlaliki 3:2 - Buku Lopatulika mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 mphindi yakubadwa ndi mphindi yakumwalira; mphindi yakubzala ndi mphindi yakuzula zobzalazo; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa pali nthaŵi yobadwa ndi nthaŵi yomwalira, pali nthaŵi yobzala ndi nthaŵi yozula zobzalazo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira, nthawi yodzala ndi nthawi yokolola. |
Koma pangano langa ndidzalimbikitsa ndi Isaki, amene Sara adzakubalira iwe nthawi yomwe ino chaka chamawa.
Ndipo nthawi inayandikira kuti Israele adzafa, ndipo anaitana Yosefe mwana wake wamwamuna, nati kwa iye, Ngati ndapeza ufulu pamaso pako, ikatu dzanja lako pansi pa ntchafu yanga, nundichitire ine zabwino ndi zoona: usandiikatu ine mu Ejipito;
Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.
Ndipo anati, Nyengo ino chaka chikudzachi udzafukata mwana wamwamuna. Koma anati, Iai, mbuyanga, munthu wa Mulungu, musanamiza mdzakazi wanu.
Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi? Ndikadayembekeza masiku onse a nkhondo yanga, mpaka kwafika kusandulika kwanga.
Popeza masiku ake alembedwa, chiwerengo cha miyezi yake chikhala ndi Inu, ndipo mwamlembera malire ake kuti asapitirirepo iye;
Kodi munthu alibe nkhondo kunja kuno? Kodi masiku ake sakunga masiku a wolembedwa ntchito?
Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse, adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako, nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo.
Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.
Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesaya mneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.
Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.
Imba, iwe wouma, amene sunabale; imba zolimba ndi kufuula zolimba, iwe amene sunabale mwana; pakuti ana a mfedwa achuluka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.
penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uononge, ugwetse, umange, ubzale.
Uzitero naye, Yehova atero: Taonani, chimene ndamanga ndidzapasula, ndi chimene ndaoka ndidzazula; ndidzatero m'dziko lonseli.
Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,
Koma Iye anayankha nati, Mmera wonse, umene Atate wanga wa Kumwamba sanaubzale, udzazulidwa.
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Ndipo taona, udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirire mau anga, amene adzakwanitsidwa pa nyengo yake.
Ndipo taona, Elizabeti mbale wako, iyenso ali ndi pakati pa mwana wamwamuna mu ukalamba wake; ndipo mwezi uno uli wachisanu ndi chimodzi wa iye amene ananenedwa wouma.
Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthawi yake; koma pamene wabala mwana, sakumbukiranso kusaukako, chifukwa cha chimwemwe kuti wabadwa munthu kudziko lapansi.
Pamenepo anafuna kumgwira Iye; koma palibe wina anamgwira kumanja, chifukwa nthawi yake siinafike.
Koma m'mene inayandikira nthawi ya lonjezo limene Mulungu adalonjezana ndi Abrahamu, anthuwo anakula nachuluka mu Ejipito,
Nyengo yomweyo anabadwa Mose, ndiye wokoma ndithu pamaso pa Mulungu; ndipo anamlera miyezi itatu m'nyumba ya atate wake:
koma pokwaniridwa nthawi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi, wobadwa wakumvera lamulo,
Amene anakhuta anakasuma chakudya; koma anjalawo anachira; inde chumba chabala asanu ndi awiri; ndipo iye amene ali ndi ana ambiri achita liwondewonde.