Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti, Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru?
Mlaliki 2:16 - Buku Lopatulika Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pakuti munthu wanzeru, pamodzi ndi chitsiru chomwe, onsewo sakumbukika nthaŵi yaitali, pokhala kuti pa masiku akutsogolo, onsewo adzaiŵalika. M'mene chimafera chitsiru ndi m'menenso amafera munthu wanzeru. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti munthu wanzeru, pamodzinso ndi chitsiru sadzakumbukiridwa nthawi yayitali; mʼmasiku amʼtsogolo awiriwo adzayiwalika. Mmene chimafera chitsiru ndi mmenenso amafera wanzeru! |
Ndipo mfumu inanenera Abinere nyimbo iyi ya maliro, niti, Kodi Abinere anayenera kufa ngati chitsiru?
Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.
Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.
Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.
Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.
Pamenepo ndinati mumtima mwanga, Chomwe chigwera chitsiru nanenso chindigwera; nanga bwanji ndinapambana kukhala wanzeru? Pamenepo ndinati mumtima mwanga kuti ichinso ndi chabe.
Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani?
Kunka kunyumba ya maliro kupambana kunka kunyumba ya madyerero; pakuti kujako ndi matsiriziro a anthu onse; ndipo omwe ali ndi moyo adzakumbukirapo.
Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumzinda nawaiwala; ichinso ndi chabe.
koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mzindawo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.
Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.
Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.