Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.
Mlaliki 2:12 - Buku Lopatulika Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndinatembenuka kukayang'ana nzeru ndi misala ndi utsiru; pakuti yemwe angotsata mfumu angachite chiyani? Si chomwe chinachitidwa kale. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo ndidayesanso kulingalira kuti kwenikweni nzeru nchiyani, misala nchiyani, uchitsiru nchiyani. Kodi munthu wodzaloŵa ufumu tsopanoyo angapose bwanji mnzake adapita uja? Nzokhazokhazo zomwe ameneyo adazichita kale. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka maganizo anga anayamba kulingalira zakuti nzeru nʼchiyani, komanso kuti misala ndi uchitsiru nʼchiyani. Kodi munthu wodzalowa ufumu tsopanoyo angachite chiyani choposa chimene chinachitidwa kale? |
Ndipo ndinapereka mtima kudziwa nzeru ndi kudziwa misala ndi utsiru; ndinazindikira kuti ichinso chingosautsa mtima.
Chomwe chinaoneka, chilikuonekabe; ndi chomwe chidzaoneka chinachitidwa kale; Mulungu anasanthula zochitidwa kale.
Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;