Mlaliki 11:7 - Buku Lopatulika Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Indetu kuunika nkokoma, maso napeza bwino m'kuona dzuwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kuŵala kwam'maŵa kumasangalatsa, ndipo maso ako akaona dzuŵa amakondwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kuwala nʼkwabwino, ndipo maso amasangalala kuona dzuwa. |
Pakuti mwalanditsa moyo wanga kuimfa, simunatero nao mapazi anga kuti ndingagwe? Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu m'kuunika kwa amoyo.
Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.
ngakhale lisanade dzuwa, ndi kuunika, ndi mwezi, ndi nyenyezi, mitambo ndi kubweranso italeka mvula;
kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.