Mlaliki 11:4 - Buku Lopatulika Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Woyang'ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Amene ayembekeza kuti mphepo ikhale bwino, kapena kuti mitambo ibwere bwino, sadzabzala ndipo sadzakolola kanthu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Amene amayangʼana mphepo sadzadzala; amene amayangʼana mitambo sadzakolola. |
Mitambo ikadzala mvula, itsanulira pansi; mtengo ukagwa kumwera pena kumpoto, pomwe unagwa mtengowo udzakhala pomwepo.
Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.