Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.
Mlaliki 10:2 - Buku Lopatulika Wanzeru, mtima wake uli kudzanja lake lamanja; koma chitsiru, mtima wake kulamanzere. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Wanzeru, mtima wake uli kudzanja lake lamanja; koma chitsiru, mtima wake kulamanzere. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mtima wa munthu wanzeru umamtsogolera bwino, koma mtima wa munthu wopusa umamsokeza. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera bwino, koma mtima wa munthu wopusa umamusocheretsa. |
Nzeru ya wochenjera ndiyo yakuti azindikire njira yake; koma utsiru wa opusa ndiwo chinyengo.
Chitsulo chikakhala chosathwa, ndipo ukaleka kunola, uzipambana kulimbikira; koma nzeru ipindulira pochenjeza.
Chitsiru chichulukitsanso mau; koma munthu sadziwa chimene chidzaoneka; ndipo ndani angamuuze chomwe chidzakhala m'tsogolo mwake?
Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.
Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.
Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu.