Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.
Mlaliki 1:8 - Buku Lopatulika Zinthu zonse zilemetsa; munthu sangathe kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Zinthu zonse zilemetsa; munthu sakhoza kuzifotokoza; maso sakhuta m'kuona, ndi makutu sakhuta m'kumva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Zinthu zonse nzolemetsa, kulemera kwake nkosasimbika. Maso sakhuta nkupenya, makutunso sakhuta nkumva. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Zinthu zonse ndi zotopetsa, kutopetsa kwake ndi kosaneneka. Maso satopa ndi kuona kapena khutu kukwaniritsidwa ndi kumva. |
Mudzakhutitsa moyo wanga ngati ndi mafuta ndi zonona; ndipo pakamwa panga ndidzakulemekezani ndi milomo yakufuula mokondwera.
Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.
Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.
Pakuti yemwe Mulungu amuyesa wabwino ampatsa nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe; koma wochimwa amlawitsa vuto la kusonkhanitsa ndi kukundika, kuti aperekere yemwe Mulungu amuyesa wabwino. Ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.
Munayembekezera zambiri, koma taonani, pang'ono; ndipo, mutabwera napo kwanu, ndinauzirapo. Chifukwa ninji? Ati Yehova wa makamu. Chifukwa cha nyumba yanga yokhala yopasuka, ndipo nuthamangira yense kunyumba kwake.