Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mlaliki 1:6 - Buku Lopatulika

Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Kulowa kumwera ndi kuzungulira kumpoto zungulirezungulire imaomba mphepo; ibweranso monga mwa mazunguliridwe ake.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mphepo imaombera chakumwera, nkudzakhotera chakumpoto. Imaomba mozungulirazungulira, pozungulirapo nkudzabwereranso komwe yachokera.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mphepo imawombera cha kummwera ndi kukhotera cha kumpoto; imawomba mozungulirazungulira, kumangobwererabwerera komwe yachokera.

Onani mutuwo



Mlaliki 1:6
11 Mawu Ofanana  

Kodi mudziwa umo zovala zanu zifundira, pamene dziko lili thuu chifukwa cha mwera?


M'chipinda mwake mutuluka kamvulumvulu, ndi chisanu chifuma kumpoto.


Popeza anena, nautsa namondwe, amene autsa mafunde ake.


Asanduliza namondwe akhale bata, kotero kuti mafunde ake atonthole.


Mitsinje yonse ithira m'nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.


Monga sudziwa njira ya mphepo, ngakhale makulidwe a mafupa m'mimba ya mkazi ali ndi pakati; momwemo sudziwa ntchito za Mulungu amene achita zonse.


Koma Yehova anautsa chimphepo chachikulu panyanja, ndipo panali namondwe wamkulu panyanja, ndi chombo chikadasweka.


Chifukwa chimenechi yense amene akamva mau anga amenewa, ndi kuwachita, ndidzamfanizira iye ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe;


ndipo inagwa mvula, nidzala mitsinje, ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumbayo; ndipo inagwa; ndi kugwa kwake kunali kwakukulu.


Mphepo iomba pomwe ifuna, ndipo ukumva mau ake, koma sudziwa kumene ichokera, ndi kumene imuka; chotero aliyense wobadwa mwa Mzimu.