Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.
Mlaliki 1:5 - Buku Lopatulika Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Inde dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira komwe linatulukako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Dzuŵa limatuluka, nkukaloŵa, ndipo limapita mwamsanga kumene linatulukira. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Dzuwa limatuluka ndipo dzuwa limalowa ndipo limapita mwamsanga kumene limatulukira. |
Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthawi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekai.
Monga nswala ipuma wefuwefu kukhumba mitsinje; motero moyo wanga upuma wefuwefu kukhumba Inu, Mulungu.
mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake.
Pakuti Yehova atero: Ngati mukhoza kuswa pangano langa la usana ndi pangano langa la usiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku, m'nyengo yao;
Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.