Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.
Mlaliki 1:4 - Buku Lopatulika Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbadwo wina ukutha, wina ukudza, koma dziko lapansi limakhalapobe losasinthika. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mibado imabwera ndipo mibado imapita, koma dziko lapansi limakhalapobe nthawi zonse. |
Ndipo Yakobo anati kwa Farao, Masiku a zaka za ulendo wanga ndi zaka zana limodzi kudza makumi atatu; masiku a zaka za moyo wanga ali owerengeka ndi oipa, sanafikire masiku a zaka za moyo wa makolo anga m'masiku a ulendo wao.
Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?