Mlaliki 1:1 - Buku Lopatulika Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya mu Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya m'Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Naŵa mau a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu: Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mawu a Mlaliki, mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu: |
Ndiponso waika aneneri akubukitsa za iwe ku Yerusalemu, ndi kuti, Ku Yuda kuli mfumu, ndipo zidzamveka kwa mfumu, kuti kuli zotere. Tiyeni tsono tipangane pamodzi.
Ndalalikira chilungamo mu msonkhano waukulu; onani, sindidzaletsa milomo yanga, mudziwa ndinu Yehova.
Taonani, ichi ndachipeza, ati Mlalikiyo, m'kuphatikiza chinthu china ndi chinzake, ndikazindikire malongosoledwe ao;
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;
ndipo sanalekerere dziko lapansi lakale, koma anasunga Nowa mlaliki wa chilungamo, ndi anzake asanu ndi awiri, pakulitengera dziko la osapembedza chigumula;