Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu.
Mika 7:19 - Buku Lopatulika Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Adzabwera, nadzatichitira nsoni; adzagonjetsa mphulupulu zathu; ndipo mudzataya zochimwa zao zonse m'nyanja yakuya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu mudzatichitiranso chifundo; mudzapondereza pansi machimo athu ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja. |
Ndipo Davide ananena ndi Gadi, Ndipsinjika mtima kwambiri, tigwe m'dzanja la Yehova; pakuti zifundo zake nzazikulu; koma tisagwe m'dzanja la munthu.
Monga kum'mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.
Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m'menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao.
Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.
Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.
Kodi Efuremu ndiye mwana wanga wokondedwa? Kodi ndiye mwana wokondweretsa? Nthawi zonse zoti ndimnenera zomtsutsa, pakuti ndimkumbukiranso ndithu; chifukwa chake mumtima mwanga ndimlirira; ndidzamchitiradi chifundo, ati Yehova.
ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.
Ndipo ndidzawayeretsa kuchotsa mphulupulu yao, imene anandichimwira Ine; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu zao zimene anandichimwira, nandilakwira Ine.
Masiku omwewo, nthawi yomweyo, ati Yehova, zoipa za Israele zidzafunidwa, koma zidzasoweka; ndi zochimwa za Yuda, koma sizidzapezeka; pakuti ndidzakhululukira iwo amene ndidzawasiya ngati chotsala.
Nnena chimodzi chonse cha zolakwa zake zonse adazichita chidzakumbukika chimtsutse; m'chilungamo chake adachichita adakhala ndi moyo.
Ndipo sindidzawabisiranso nkhope yanga, popeza ndatsanulira mzimu wanga pa nyumba ya Israele, ati Ambuye Yehova.
Masabata makumi asanu ndi awiri alamulidwira anthu a mtundu wako ndi mzinda wako wopatulika, kumaliza cholakwacho, ndi kutsiriza machimo, ndi kutetezera mphulupulu, ndi kufikitsa chilungamo chosalekeza, ndi kukhomera chizindikiro masomphenya ndi zonenera, ndi kudzoza malo opatulika kwambiri.
Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe.
Ndipo Iye anayankha nanena ndi iwo akuima pamaso pake, ndi kuti, Mumvule nsalu zonyansazi. Nati kwa iye, Taona, ndakuchotsera mphulupulu zako, ndipo ndidzakuveka zovala za mtengo wake.
pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.
pamenepo Yehova Mulungu wanu adzauchotsa ukapolo wanu, ndi kukuchitirani chifundo; nadzabwera ndi kukumemezani mwa mitundu yonse ya anthu, kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsiraniko.
Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudulani mtima wanu, ndi mtima wa mbeu zanu, kuti mukonde Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, kuti mukhale ndi moyo.
Popeza Yehova adzaweruza anthu ake, nadzachitira nsoni anthu ake; pakuona Iye kuti mphamvu yao yatha, wosatsala womangika kapena waufulu.
amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole ife kuzoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ake enieni, achangu pa ntchito zokoma.
iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.