Mika 6:11 - Buku Lopatulika Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi ndingathe kulekerera munthu amene ali ndi sikelo zobera anzake ndiponso miyeso yonyenga? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo, ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake? |
Mwini muyeso ndi mulingo wolungama ndiye Yehova; ndiyenso anapanga miyala yonse yoyesera ya m'thumba.
Mukhale nacho choyesera choona, miyeso yoona, efa woona, hini woona; Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito.
Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;
Ndipo anati, Uyu ndi uchimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntovu wolemerawo pakamwa pake.