Mika 6:10 - Buku Lopatulika Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi Ine ndingathe kuiŵala chuma chimene chili m'nyumba za anthu oipa, chimene adachipata monyenga, ndiponso muyeso wopereŵera umene uli wotembereredwa? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo, ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa? |
Pakuti sadziwa kuchita zolungama, amene akundika zachiwawa ndi umbala m'nyumba zao zachifumu, ati Yehova.
Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero aakulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.
Mau a Yehova aitana mzinda, ndi wanzeru aopa dzina lanu; tamverani ndodo, ndi Iye amene anaiika.
Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.
Ndipo ndinati, Nchiyani ichi? Nati iye, Ichi ndi efa alikutuluka. Natinso, Ichi ndi maonekedwe ao m'dziko lonse;
Koma ana a Israele analakwa ndi choperekedwacho; popeza Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda, anatapa choperekedwacho; ndi mkwiyo wa Yehova unayakira ana a Israele.