Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira;
Mika 5:14 - Buku Lopatulika Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha mizinda yako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ndidzazula zifanizo zako m'kati mwako, ndi kutha midzi yako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzagwetsa mafano anu a Asera m'dziko mwanu, ndipo ndidzaononga mizinda yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu, ndipo ndidzawononga mizinda yanu. |
Nadziimikira zoimiritsa ndi zifanizo pa chitunda chilichonse chachitali, ndi patsinde pa mtengo uliwonse wogudira;
koma mupasule maguwa a nsembe ao, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao;
Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.
Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.
Koma ngati sakumva, ndidzazula mtundu umene wa anthu, kuuzula ndi kuuononga, ati Yehova.
Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.
Ndipo Yehova walamulira za iwe kuti asabzalidwenso ena a dzina lako; m'nyumba ya milungu yako ndidzachotsa fano losema ndi fano loyenga; ndidzakukonzerapo manda, pakuti iwe ndiwe wopepuka.