Dziko lanu lili bwinja; mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.
Mika 5:11 - Buku Lopatulika ndipo ndidzaononga mizinda ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo ndidzaononga midzi ya m'dziko lako, ndi kupasula malinga ako onse; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidzaononga mizinda ya m'dziko mwanu ndi kugwetseratu malinga anu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzawononga mizinda ya mʼdziko mwanu ndi kugwetsa malinga anu onse. |
Dziko lanu lili bwinja; mizinda yanu yatenthedwa ndi moto; dziko lanu alendo alimkudya pamaso panu; ndipo lili labwinja monga lagubuduzidwa ndi alendo.
Chifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, chifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a achilendo.
Chifukwa chake, mwa ichi choipa cha Yakobo chidzafafanizidwa, ndipo ichi ndi chipatso chonse chakuchotsa tchimo lake; pamene iye adzayesa miyala yonse ya guwa la nsembe, ngati miyala yanjeresa yoswekasweka, zifanizo ndi mafano a dzuwa sizidzaukanso konse.
Pompo ndinati ine, Ambuye mpaka liti? Ndipo anayankha, Mpaka mizinda ikhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda munthu, ndi dziko likhala bwinja ndithu,
Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.
nudzati, Ndidzakwera kunka kudziko la midzi yopanda malinga, ndidzanka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka, onsewo akukhala opanda malinga, opanda mapiringidzo, kapena zitseko;
Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribele; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ake.
Pamenepo anayankha, nanena kwa ine, ndi kuti, Awa ndi mau a Yehova kwa Zerubabele, Ndi khamu la nkhondo ai, ndi mphamvu ai, koma ndi Mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.