Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mika 5:10 - Buku Lopatulika

Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m'kati mwako, ndi kutha magaleta ako;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo kudzachitika tsiku ilo, ati Yehova, ndidzaononga akavalo ako m'kati mwako, ndi kutha magaleta ako;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Komabe Chauta akuuza Aisraele kuti, “Pa tsiku limenelo ndidzaononga akavalo anu onse, ndipo ndidzaphwasula magaleta anu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yehova akuti, “Tsiku limenelo ndidzawononga akavalo anu onse ndi kuphwasula magaleta anu.

Onani mutuwo



Mika 5:10
9 Mawu Ofanana  

Dziko lao ladzala siliva ndi golide, ngakhale chuma chao nchosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magaleta ao ngosawerengeka.


Ndithu akhulupirira mwachabe chithandizo cha kuzitunda, ndi phokoso la kumapiri; ndithu mwa Yehova Mulungu wathu muli chipulumutso cha Israele.


Koma ndidzachitira chifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.


Asiriya sadzatipulumutsa; sitidzayenda pa akavalo, ndipo sitidzanenanso kwa ntchito ya manja athu, Inu ndinu milungu yathu; pakuti mwa Inu ana amasiye apeza chifundo.


ndipo ndidzagubuduza mipando yachifumu ya maufumu, ndidzaononga mphamvu ya maufumu a amitundu; ndidzagubuduza magaleta ndi iwo akuyendapo; ndi akavalo ndi apakavalo adzatsika, yense ndi lupanga la mbale wake.


Ndipo ndidzaononga magaleta kuwachotsa mu Efuremu, ndi akavalo kuwachotsa mu Yerusalemu; ndi uta wa nkhondo udzaonongeka; ndipo adzanena zamtendere kwa amitundu; ndi ufumu wake udzakhala kuyambira kunyanja kufikira nyanja, ndi kuyambira ku Mtsinje kufikira malekezero a dziko.


Koma asadzichulukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu anke ku Ejipito, kuti achulukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.