Mika 3:12 - Buku Lopatulika Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi m'Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono chifukwa cha inu Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho chifukwa cha inu, Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira. |
Mulungu, akunja alowa m'cholowa chanu; anaipsa Kachisi wanu woyera; anachititsa Yerusalemu bwinja.
pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mzinda wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;
Iwe phiri langa la m'munda, ndidzapereka chuma chako ndi zosungidwa zako zikafunkhidwe, ndi misanje yako, chifukwa cha tchimo, m'malire ako onse.
Koma ngati simudzamva mau amenewa, Ine ndilumbira, pali Ine mwini, ati Yehova, nyumba iyi idzakhala yabwinja.
Pakuti Yehova atero za nyumba ya mfumu ya Yuda: Ndikuyesa iwe Giliyadi, ndi mutu wa Lebanoni; koma ndidzakuyesa iwe chipululu, ndi mizinda yosakhalamo anthu.
Mika Mmoreseti ananenera masiku a Hezekiya mfumu ya Yuda; ndipo iye ananena kwa anthu onse a Yuda, kuti, Yehova wa makamu atero: Ziyoni adzalimidwa ngati munda, Yerusalemu adzakhala miunda, ndi phiri la nyumba longa misanje ya nkhalango.
Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzafikitsa pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu choipa chonsecho ndawanenera iwo; chifukwa ndanena ndi iwo, koma sanamve; ndaitana, koma iwo sanandivomere.
Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Mwaona choipa chonse chimene ndatengera pa Yerusalemu, ndi pa mizinda yonse ya Yuda; ndipo, taonani, lero lomwe ili bwinja, palibe munthu wokhalamo;
ndipo anatentha nyumba ya Yehova ndi nyumba ya mfumu, ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu, ngakhale zinyumba zazikulu zonse, anazitentha ndi moto.
Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.
Ndipo ndidzayesa Yerusalemu miyulu, mbuto ya ankhandwe; ndipo ndidzayesa mizinda ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.
Chifukwa chake ndidzaika Samariya ngati mulu wa miyala ya m'munda, ngati zooka m'munda wampesa; ndipo ndidzataya miyala yake m'chigwa, ndi kufukula maziko ake.
Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.