Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mzinda wokhetsa mwazi pakati pake kuti nthawi yake ifike, nudzipangire mafano udzidetsa nao.
Mika 3:10 - Buku Lopatulika Amanga Ziyoni ndi mwazi, ndi Yerusalemu ndi chisalungamo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Amanga Ziyoni ndi mwazi, ndi Yerusalemu ndi chisalungamo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumamanga Ziyoni ndi chuma chochipata pakupha anthu, Yerusalemu mumammanga ndi kuipa kwanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero inu amene mukumanga Ziyoni pokhetsa magazi, ndi Yerusalemu ndi kuyipa kwanu. |
Nuziti, Atero Ambuye Yehova, Ndiwo mzinda wokhetsa mwazi pakati pake kuti nthawi yake ifike, nudzipangire mafano udzidetsa nao.
Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.
Akalonga ake m'kati mwake ndiwo mikango yobangula; oweruza ake ndi mimbulu ya madzulo, sasiya kanthu ka mawa.
kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke.