Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?
Mika 2:8 - Buku Lopatulika Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma ngakhale dzulo anthu anga anauka ngati mdani; mukwatula chofunda kumalaya a iwo opitirira mosatekeseka, ngati anthu osafuna nkhondo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chauta akuti, “Koma inu mumaukira anthu anga ngati mdani. Mumaŵavula mkanjo anthu amtendere, amene amangoyenda ndi mtima wokhazikika, osaganizako za nkhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Posachedwapa anthu anga andiwukira ngati mdani. Mumawavula mkanjo wamtengowapatali anthu amene amadutsa mosaopa kanthu, monga anthu amene akubwera ku nkhondo. |
Ine ndine wa awo amene ali amtendere ndi okhulupirika mu Israele; inu mulikufuna kuononga mzinda ndi mai wa mu Israele; mudzamezeranji cholowa cha Yehova?
Manase adzadya Efuremu; ndi Efuremu adzadya Manase, ndipo iwo pamodzi adzadyana ndi Yuda. Mwa izi zonse mkwiyo wake sunachoke, koma dzanja lake lili chitambasulire.
Cholowa changa chandisandukira mkango wa m'nkhalango; anatsutsana nane ndi mau ake; chifukwa chake ndinamuda.
Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;
inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lao ndi kuthyola mafupa ao; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.
Watha wachifundo m'dziko, palibe woongoka mwa anthu; onsewo alalira mwazi; yense asaka mbale wake ndi ukonde.
Manja ao onse awiri agwira choipa kuchichita ndi changu; kalonga apempha, ndi woweruza aweruza chifukwa cha mphotho; ndi wamkuluyo angonena chosakaza moyo wake; ndipo achiluka pamodzi.