Sitiziona zizindikiro zathu; palibenso mneneri; ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.
Mika 2:6 - Buku Lopatulika Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musamanenera, amanenera ati. Sadzanenera kwa awa; matonzo sadzachoka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu amandiwuza kuti, “Musatilalikire, munthu asalalike zimenezi. Manyazi sadzatigwera ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere! Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi; ife sitidzachititsidwa manyazi.” |
Sitiziona zizindikiro zathu; palibenso mneneri; ndipo mwa ife palibe wina wakudziwa mpaka liti.
Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli.
amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;
Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako njira ya kumwera, nubenthulire mau kumwera, nunenere nkhalango yakuthengo la kumwera kwa Yuda;
Wobadwa ndi munthu iwe, lozetsa nkhope yako ku Yerusalemu, nuwabenthulire mau malo opatulikawa, nunenere dziko la Israele kulitsutsa;
ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.
koma usaneneranso ku Betele; pakuti pamenepo mpamalo opatulika a mfumu, ndiyo nyumba yachifumu.
Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki;
chifukwa chake kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuwa lidzalowera aneneri, ndi usana udzawadera bii.
Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.
Komatu tiwaopse asalankhulenso m'dzina ili kwa munthu aliyense, kuti chisabukenso kwa anthu.
nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.
Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m'mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.
Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.