Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira.
Mika 1:15 - Buku Lopatulika Ndidzakutengeranso wokhala mu Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzakutengeranso wokhala m'Maresa iwe, iye amene adzakulandira ukhale cholowa chake; ulemerero wa Israele udzafikira ku Adulamu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inunso anthu a ku Maresa, ndidzakutumirani adani kuti akugonjetseni. Akuluakulu a ku Israele adzabisala m'thanthwe la Adulamu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu okhala mu Maresa. Ulemerero wa Israeli udzafika ku Adulamu. |
Ndipo panali nthawi yomweyo, kuti Yuda anatsikira kwa abale ake nalowa kwa Mwadulamu, dzina lake Hira.
Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m'chigwa cha Refaimu.
Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?
Za ana a Amoni. Yehova atero: Kodi Israele alibe ana aamuna? Alibe wolowa dzina? M'mwemo mfumu yao yalowa pa Gadi chifukwa chanji, ndi anthu ake akhala m'mizinda mwake?
Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.