Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mika 1:14 - Buku Lopatulika

Chifukwa chake pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti-Gati; nyumba za Akizibu zidzakhala chinthu chabodza kwa mafumu a Israele.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Chifukwa chake pereka mphatso zolawirana kwa Moreseti-Gati; nyumba za Akizibu zidzakhala chinthu chabodza kwa mafumu a Israele.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono a ku Moreseti-Gati mutsazikane nawo. Anthu a ku Akizibu adzanamiza mafumu a ku Israele.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana ndi a ku Moreseti Gati. Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama kwa mafumu a Israeli.

Onani mutuwo



Mika 1:14
10 Mawu Ofanana  

Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.


Natenga Ahazi siliva ndi golide wopezeka m'nyumba ya Yehova, ndi ku chuma cha nyumba ya mfumu, nazitumiza mtulo kwa mfumu ya Asiriya.


Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.


Katundu wa zilombo za kumwera. M'dziko lovuta ndi lopweteka, kumeneko kuchokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula chuma chao pamsana pa abulu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamira, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.


Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?


ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao.