Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasekere, kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.
Mika 1:10 - Buku Lopatulika Musachifotokoza mu Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Musachifotokoza m'Gati, musalira misozi konse; m'nyumba ya Afira ndinagubuduka m'fumbi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musaŵauze zimenezi a ku Gati, musalire konse. Muvimvinizike m'fumbi ku Beteleafura, kuwonetsa chisoni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musanene zimenezi ku Gati; musalire nʼkomwe. Mugubuduzike mu fumbi ku Beti-Leafura. |
Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasekere, kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.
Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, udziveke ndi chiguduli, ndi kumvimvinika m'phulusa; ulire maliro ngati a mwana wamwamuna wa yekha, kulira kowawa koposa; pakuti wakufunkha adzatifikira ife motidzidzimutsa.
Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova.