Mateyu 9:30 - Buku Lopatulika Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo maso ao anaphenyuka. Ndipo Yesu anawauzitsa iwo, nanena, Yang'anirani, asadziwe munthu aliyense. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo maso ao adaphenyuka. Tsono Yesu adaŵalamula mwamphamvu kuti, “Wina aliyense asazidziŵetu zimenezi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati, “Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi.” |
kuti utsegule maso akhungu, utulutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m'nyumba ya kaidi.
Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.
Ndipo pamene anali kutsika paphiri, Yesu anawalamula iwo kuti, Musakauze munthu choonekacho, kufikira Mwana wa Munthu adadzauka kwa akufa.
Ndipo Yesu ananena naye, Ona, iwe, usauze munthu; koma muka, udzionetse wekha kwa wansembe, nupereke mtulo umene anaulamulira Mose, ukhale mboni kwa iwo.
Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.
Ndipo Iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.
Ndipo atate wake ndi amake anadabwa; ndipo analamulira iwo asauze munthu aliyense chimene chinachitika.