Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.
Mateyu 9:29 - Buku Lopatulika Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo anakhudza maso ao, nati, Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiriro chanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Yesu adakhudza maso ao nati, “Zikuchitikireni monga momwe mwakhulupiriramo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pomwepo anakhudza maso awo nati, “Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu.” |
Pomwepo Yesu anayankha, nati kwa iye, Mkaziwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu; chikhale kwa iwe monga momwe wafunira. Ndipo mwana wake anachira nthawi yomweyo.
Ndipo Yesu anagwidwa ndi chifundo, nakhudza maso ao; ndipo pomwepo anapenyanso, namtsata Iye.
Ndipo Yesu anati kwa kenturiyoyo, Pita, kukhale kwa iwe monga unakhulupirira. Ndipo anachiritsidwa mnyamatayo nthawi yomweyo.
Koma Yesu potembenuka ndi kuona iye anati, Limba mtima, mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Ndipo mkaziyo anachira kuyambira nthawi yomweyo.
Ndipo m'mene Iye analowa m'nyumbamo, akhunguwo anadza kwa Iye; ndipo Yesu anati kwa iwo, Mukhulupirira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi? Anena kwa Iye, Inde, Ambuye.
Ndipo Yesu anati kwa iye, Muka; chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe. Ndipo pomwepo anapenyanso; namtsata Iye panjira.