Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Mateyu 9:26 - Buku Lopatulika Ndipo mbiri yake imene inabuka m'dziko lonse limenelo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mbiri yake imene inabuka m'dziko lonse limenelo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mbiri imeneyi idawanda m'dera lonselo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mbiriyi inamveka mʼdera lonse. |
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m'mudzi, koma anakhala padera m'mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.
Ndipo mfumu Herode anamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.
Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.
Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao.
Pakuti mfumuyo idziwa izi, kwa iye imene ndilankhula nayonso mosaopa: pakuti ndidziwadi kuti kulibe kanthu ka izi kadambisikira; pakuti ichi sichinachitike m'tseri.