ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.
Mateyu 9:21 - Buku Lopatulika pakuti analikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chofunda chake chokha ndidzachira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti analikunena mwa iye yekha, Ngati ndingakhudze chofunda chake chokha ndidzachira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale chovala chake chokhacho, ndichira.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iyeyo anati mwa iye yekha, “Nditangokhudza kasonga ka mkanjo wake, ine ndidzachiritsidwa.” |
ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.
pakuti adawachiritsa ambiri; kotero kuti onse akukhala nazo zowawa anakanikiza Iye, kuti akamkhudze.
ndi khamu lonse lija linafuna kumkhudza Iye; chifukwa munatuluka mphamvu mwa Iye, nkuchiritsa onsewa.
kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.