Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 9:20 - Buku Lopatulika

Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Panali mayi wina amene ankadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri ndipo anadza mʼmbuyo mwake nakhudza mkanjo wake.

Onani mutuwo



Mateyu 9:20
12 Mawu Ofanana  

ndipo anampempha Iye, kuti akhudze mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.


Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,


Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe.


Ndipo kumene konse adalowa Iye m'midzi, kapena m'mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.


Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze.


kotero kuti anamuka nazo kwa odwala nsalu zopukutira ndi za pantchito, zochokera pathupi pake, ndipo nthenda zinawachokera, ndi ziwanda zinatuluka.


kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.


Mudzipangire mphonje pangodya zinai za chofunda chanu chimene mudzifunda nacho.