Mateyu 9:19 - Buku Lopatulika Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yesu ananyamuka namtsata iye, ndi ophunzira ake omwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo Yesu adanyamuka, namtsatira pamodzi ndi ophunzira ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu ndi ophunzira ake ananyamuka napita naye pamodzi. |
M'mene Iye analikulankhula nao zinthu zimenezo, onani, anadza munthu mkulu, namgwadira Iye, nanena, Wamwalira tsopanoli mwana wanga wamkazi, komatu mudze muike dzanja lanu pa iye, ndipo adzakhala ndi moyo.
Ndipo onani, mkazi, anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri, anadza pambuyo pake, nakhudza mphonje ya chofunda chake;
Yesu ananena nao, Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.
za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.