Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?
Mateyu 9:14 - Buku Lopatulika Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawirikawiri, koma ophunzira anu sasala? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo anadza kwa Iye ophunzira ake a Yohane, nati, Chifukwa ninji ife ndi Afarisi tisala kudya kawirikawiri, koma ophunzira anu sasala? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake ophunzira a Yohane Mbatizi adabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ife ndi Afarisi timasala zakudya kaŵirikaŵiri, pamene ophunzira anu sasala nkomwe?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ophunzira a Yohane anabwera namufunsa Iye kuti, “Bwanji ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?” |
Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?
Koma Yohane, pakumva m'nyumba yandende ntchito za Khristu, anatumiza ophunzira ake mau,
Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.
Ndipo Yesu anati kwa iwo, Nanga anyamata a nyumba ya ukwati angathe kulira kodi nthawi imene mkwati akhala nao? Koma adzafika masiku, pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, ndipo pomwepo adzasala kudya.
Chifukwa chake pamene Ambuye anadziwa kuti Afarisi adamva kuti Yesu anayesa anthu ophunzira, nawabatiza koposa Yohane