Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?
Mateyu 9:10 - Buku Lopatulika Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali pamene Iye analinkukhala pachakudya m'nyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anadza nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba, kudabwera anthu ambiri okhometsa msonkho, ndi anthu ochimwa, kudzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo pamene Iye ankadya mʼnyumba, onani, amisonkho ndi ochimwa ambiri anabwera nakhala pansi pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. |
Ndipo Afarisi, pakuona ichi, ananena kwa ophunzira ake, Chifukwa ninji Mphunzitsi wanu alinkudya pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?
Ndipo Yesu popita, kuchokera kumeneko, anaona munthu, dzina lake Mateyu, alinkukhala polandirira msonkho, nanena kwa iye, Nditsate Ine. Ndipo iye anauka, namtsata.
Tidziwa kuti Mulungu samvera ochimwa. Koma ngati munthu aliyense akhala wopembedza Mulungu nachita chifuniro chake, amvera ameneyo.