Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Mateyu 8:31 - Buku Lopatulika Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mizimuyo inampempha Iye ninena, Ngati mutitulutsa, mutitumize ife tilowe m'gulu la nkhumbazo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti, “Mukatitulutsa, bwanji mutitume kuti tikaloŵe m'gulu la nkhumba zili apozo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ziwandazo zinamupempha Yesu kuti, “Ngati mutitulutsa ife mutitumize mu nkhumba izo.” |
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Musamapatsa chopatulikacho kwa agalu, ndipo musamaponya ngale zanu patsogolo pa nkhumba, kuti zingazipondereze ndi mapazi ao, ndi potembenuka zingang'ambe inu.
Ndipo anati kwa iyo, Mukani. Ndipo inatuluka, nimuka, kukalowa m'nkhumbazo; ndipo onani, gulu lonse linathamangira kunsi kuphompho m'nyanjamo, ndipo linafa m'madzi.
ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.
Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.