Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Mateyu 8:23 - Buku Lopatulika

Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ake anamtsata Iye.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo pamene Iye atalowa m'ngalawa, ophunzira ake anamtsata Iye.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu adaloŵa m'chombo, ndipo ophunzira ake adatsagana naye.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye atalowa mʼbwato, ophunzira ake anamutsatira.

Onani mutuwo



Mateyu 8:23
6 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, panauka namondwe wamkulu panyanja, kotero kuti ngalawa inafundidwa ndi mafunde: koma Iye anali m'tulo.


Ndipo Iye analowa m'ngalawa, naoloka, nadza kumzinda kwao.


Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere tsidya lina.


Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhate akonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.