Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.
Mateyu 8:21 - Buku Lopatulika Ndipo wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine ndiyambe ndamuka kuika maliro a atate wanga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, mundilole ine nditange ndamuka kuika maliro a atate wanga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wophunzira wake wina adauza Yesu kuti, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakaika maliro a atate anga.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Wophunzira wina anati kwa Iye, “Ambuye, mundilole ndiyambe ndakayika maliro a abambo anga.” |
Atero Yehova wa makamu, akuti, Anthu awa anena, Nthawi siinafike, nthawi yakumanga nyumba ya Yehova.
Ndipo onse amene adasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena atate, kapena amai, kapena ana, kapena minda, chifukwa cha dzina langa, adzalandira zobwezeredwa zambirimbiri, nadzalowa moyo wosatha.
Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.
Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Khristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.